21 Tsopano, kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanga ndi mmene ine ndilili, Tukiko,+ mʼbale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupirika wa Ambuye, adzakufotokozerani zonse.+ 22 Ndamutumiza kwa inu ndi cholinga chimenechi, kuti mudziwe za moyo wathu ndiponso kuti atonthoze mitima yanu.