-
Aefeso 5:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Nkhani zachiwerewere* komanso chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe nʼkomwe pakati panu,+ chifukwa anthu oyera sayenera kuchita zimenezi.+ 4 Musatchule ngakhale nkhani zokhudza khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana+ chifukwa ndi zinthu zosayenera. Mʼmalomwake muziyamika Mulungu.+
-