-
Genesis 1:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu mʼchifaniziro+ chathu, kuti akhale wofanana nafe.+ Ayangʼanire nsomba zamʼnyanja, zamoyo zouluka mumlengalenga, nyama zoweta ndiponso nyama iliyonse yokwawa padziko lapansi. Komanso asamalire dziko lonse lapansi.”+ 27 Choncho Mulungu analenga munthu mʼchifaniziro chake, mʼchifaniziro cha Mulungu analenga munthu. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+
-