-
2 Atesalonika 2:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Komabe abale, pa nkhani yokhudza kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu+ komanso kusonkhanitsidwa kwathu kwa iye,+ tikukupemphani kuti 2 musalole kuti wina aliyense asinthe maganizo anu omwe ndi olondola. Musasokonezeke ngati wina atanena kuti tsiku la Yehova*+ lafika, ngakhale atanena kuti uthengawo ndi wochokera kwa Mulungu,+ kapena atanena kuti anawerenga mʼkalata imene anthu ena akunena kuti ife ndi amene tinalemba.
-