-
Tito 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Ine Paulo, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa ndi Mulungu. Komanso ndikudziwa molondola choonadi chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu. 2 Zinthu zimenezi timakhala nazo chifukwa cha chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chimene Mulungu amene sanganame+ analonjeza kalekale.
-