28 Izi zikufanana ndi zimene Mwana wa munthu anachita. Iye sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuti awombole anthu ambiri.”+
13 Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima,+ nʼkutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Kudzera mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo* ndipo machimo athu amakhululukidwa.+