-
Levitiko 9:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo ako+ ndi a nyumba yako.* Ukatero uwaperekere nsembe anthuwa+ nʼkuwaphimbira machimo awo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”
8 Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe nʼkupha ngʼombe yaingʼono kuti ikhale nsembe yake+ yamachimo. 9 Ndiyeno ana ake anamubweretsera magazi+ a ngʼombeyo ndipo iye anaviika chala chake mʼmagaziwo nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe. Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo.+
-