17 Mu uthenga wabwinowu, Mulungu amaulula chilungamo chake kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro.+ Zikatero, chikhulupiriro cha anthuwo chimalimba mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+