-
Genesis 27:38-40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Esau anafunsa bambo ake kuti: “Bambo, ngakhale dalitso limodzi silinatsaleko? Bambo ndidalitseni, inenso ndidalitseni chonde!” Atatero Esau analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.+ 39 Koma Isaki bambo ake anamuuza kuti:
“Taona, udzakhala kutali ndi nthaka yachonde, komanso kutali ndi mame akumwamba.+ 40 Pa nthawi yonse ya moyo wako uzidzadalira lupanga+ ndipo udzatumikira mʼbale wako.+ Koma ukadzatopa ndi goli lake, udzalithyola ndi kulichotsa mʼkhosi mwako.”+
-