-
Genesis 50:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Potsirizira pake, Yosefe anauza abale ake kuti: “Ine ndikufa, koma Mulungu adzakuthandizani+ ndipo adzakutulutsani ndithu mʼdziko lino. Adzakupititsani kudziko limene analumbira kuti adzalipereka kwa Abulahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo.”+ 25 Tsopano Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeliwo kuti: “Ndithu Mulungu adzakuthandizani. Choncho mudzatenge mafupa anga pochoka kuno.”+
-