20 Ansembe aja ataliza malipenga, asilikali nʼkumva kulira kwa malipengawo, asilikaliwo anafuula mwamphamvu+ mfuu yankhondo ndipo mpanda wa mzindawo unagwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko nʼkulanda mzindawo.