3 Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+
9 Aliyense amene ali mwana wa Mulungu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo,+ chifukwa ali ndi mzimu wa Mulungu.* Ndipo sangakhale ndi chizolowezi chochita tchimo, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.+