-
Chivumbulutso 13:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndipo chinaloledwa kupereka mpweya* kwa chifaniziro cha chilombo chija, kuti chifaniziro cha chilombocho chithe kulankhula komanso kuchititsa kuti onse amene akukana kulambira chifaniziro cha chilombocho aphedwe.
16 Chilombocho chinakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti aikidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pachipumi pawo.+
-