13 Mngelo wa 6+ analiza lipenga lake.+ Ndipo ndinamva mawu amodzi kuchokera panyanga zapaguwa lansembe lagolide+ limene lili pamaso pa Mulungu, 14 akuuza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: “Masula angelo 4 amene amangidwa kumtsinje waukulu wa Firate.”+