12 Ndinacheuka kuti ndione kuti ndi ndani amene ankandilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.+ 13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi ndipo anali atamanga lamba wagolide pachifuwa.