Salimo
Iye wavala ulemerero.
Yehova wavala mphamvu
Wazivala ngati lamba wamʼchiuno.
Dziko lapansi lakhazikika,
Moti silingasunthidwe.*
3 Inu Yehova, mitsinje yasefukira,
Mitsinje yasefukira ndipo ikuchita mkokomo.
Mitsinje ikupitiriza kusefukira komanso kuchita mkokomo.
4 Ulemerero wa Yehova ndi waukulu kumwamba,
Kuposa mkokomo wa madzi ambiri,+
Ndi wamphamvu kuposa mafunde amphamvu amʼnyanja.+
5 Zikumbutso zanu ndi zodalirika kwambiri.+
Inu Yehova, nyumba yanu ndi yokongola komanso yoyera+ nthawi zonse.