1 Mbiri
25 Davide ndi atsogoleri a magulu a anthu otumikira, anasankha ena mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni+ kuti azitumikira polosera ndi azeze, zoimbira za zingwe+ ndi zinganga.+ Anthu audindo amene anawasankha kuti azichita utumiki umenewu anali awa: 2 Pa ana a Asafu, anatengapo Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asarela. Ana akewa ankatsogoleredwa ndi Asafuyo, amenenso ankalosera, ndipo ankayangʼaniridwa ndi mfumu. 3 Kwa Yedutuni,+ anatengako ana ake awa: Gedaliya, Zeri, Yesaiya, Simeyi, Hasabiya ndi Matitiya,+ onse pamodzi analipo 6. Iwowa ankayangʼaniridwa ndi Yedutuni bambo awo, amene ankalosera ndi zeze ndipo ankayamika ndi kutamanda Yehova.+ 4 Kwa Hemani,+ anatengako ana ake awa: Bukiya, Mataniya, Uziyeli, Sebueli, Yerimoti, Hananiya, Haneni, Eliyata, Gidaliti, Romamiti-ezeri, Yosebekasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti. 5 Onsewa anali ana a Hemani, wamasomphenya wa mfumu pa zinthu za Mulungu woona pofuna kutamanda Mulungu.* Choncho Mulungu woona anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu. 6 Ana onsewa ankayangʼaniridwa ndi bambo awo poimba nyimbo panyumba ya Yehova. Ankaimba nyimbozo ndi zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze,+ potumikira panyumba ya Mulungu woona.
Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani ankayangʼaniridwa ndi mfumu.
7 Chiwerengero chawo, pamodzi ndi abale awo ophunzitsidwa kuimbira Yehova, chinali 288 ndipo onse anali akatswiri. 8 Kenako anachita maere+ powagawira ntchito yoti azichita. Pochita maerewo, sankayangʼana kuti uyu ndi wamngʼono kapena wamkulu, katswiri kapena wophunzira kumene.
9 Maere oyamba anagwera Yosefe mwana wa Asafu,+ achiwiri anagwera Gedaliya+ (iye ndi abale ake ndiponso ana ake analipo 12). 10 Achitatu anagwera Zakuri,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 11 a 4 anagwera Iziri, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 12 a 5 anagwera Netaniya,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 13 a 6 anagwera Bukiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 14 a 7 anagwera Yesarela, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 15 a 8 anagwera Yesaiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 16 a 9 anagwera Mataniya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 17 a 10 anagwera Simeyi, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 18 a 11 anagwera Azareli, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 19 a 12 anagwera Hasabiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 20 a 13 anagwera Subaeli,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 21 a 14 anagwera Matitiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 22 a 15 anagwera Yeremoti, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 23 a 16 anagwera Hananiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 24 a 17 anagwera Yosebekasa, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 25 a 18 anagwera Haneni, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 26 a 19 anagwera Maloti, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 27 a 20 anagwera Eliyata, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 28 a 21 anagwera Hotiri, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 29 a 22 anagwera Gidaliti,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 30 a 23 anagwera Mahazioti,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 31 ndipo maere a 24 anagwera Romamiti-ezeri,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12.