1 Mbiri
24 Magulu a mbadwa za ana a Aroni anali awa: Ana a Aroni anali Nadabu, Abihu,+ Eliezara ndi Itamara.+ 2 Nadabu ndi Abihu anamwalira opanda ana aamuna bambo awo adakali ndi moyo,+ koma Eliezara+ ndi Itamara ankatumikirabe ngati ansembe. 3 Davide, komanso Zadoki+ yemwe anali wochokera mwa ana a Eleazara, ndiponso Ahimeleki wochokera mwa ana a Itamara, anagawa ana a Aroniwo mʼmagulu mogwirizana ndi udindo wa utumiki wawo. 4 Koma chifukwa chakuti ana a Eliezara anali ndi atsogoleri ambiri kuposa ana a Itamara, anawagawa mogwirizana ndi chiwerengero chawo. Ana a Eliezara anali ndi atsogoleri 16 a nyumba za makolo awo ndipo ana a Itamara anali ndi atsogoleri 8 a nyumba za makolo awo.
5 Pogawapo, anachita maere+ pakati pa magulu awiriwa chifukwa panali atsogoleri apamalo oyera ndi atsogoleri otumikira Mulungu woona ochokera mbali zonse ziwiri, kwa ana a Eliezara ndiponso kwa ana a Itamara. 6 Kenako Semaya mwana wa Netaneli mlembi wa Alevi, anawalemba mayina pamaso pa mfumu, akalonga, wansembe Zadoki,+ Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara+ ndiponso pamaso pa atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi. Ankasankha nyumba imodzi ya makolo kuchokera kwa ana a Eleazara kenako nʼkusankhanso nyumba imodzi ya makolo kuchokera kwa ana a Itamara.
7 Maere oyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri Yedaya, 8 achitatu Harimu, a 4 Seorimu, 9 a 5 Malikiya, a 6 Miyamini, 10 a 7 Hakozi, a 8 Abiya,+ 11 a 9 Yesuwa, a 10 Sekaniya, 12 a 11 Eliyasibu, a 12 Yakimu, 13 a 13 Hupa, a 14 Yesebeabu, 14 a 15 Biliga, a 16 Imeri, 15 a 17 Heziri, a 18 Hapizezi, 16 a 19 Petahiya, a 20 Yehezikeli, 17 a 21 Yakini, a 22 Gamuli, 18 a 23 Delaya ndipo a 24 anagwera Maaziya.
19 Umu ndi mmene ankachitira utumiki wawo+ akalowa mʼnyumba ya Yehova mogwirizana ndi dongosolo limene Aroni kholo lawo anakhazikitsa ngati mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli anamulamulira.
20 Alevi amene anatsala anali awa: Pa ana a Amuramu+ panali Subaeli.+ Pa ana a Subaeli panali Yedeya. 21 Panalinso Rehabiya.+ Pa ana a Rehabiya panali Isiya mtsogoleri wawo. 22 Pa mbadwa za Izara, panali Selomoti.+ Pa ana a Selomoti panali Yahati. 23 Ana a Heburoni anali Yeriya+ mtsogoleri wawo, Amariya wachiwiri, Yahazieli wachitatu ndi Yekameamu wa 4. 24 Pa ana a Uziyeli panali Mika. Pa ana a Mika panali Samiri. 25 Mchimwene wake wa Mika anali Isiya ndipo pa ana a Isiya panali Zekariya.
26 Ana a Merari+ anali Mali ndi Musi. Pa ana a Yaaziya panali Beno. 27 Pa ana a Merari panali Yaaziya. Ana a Yaaziya anali Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri. 28 Pa ana a Mali panali Eliezara amene analibe mwana.+ 29 Panalinso Kisi. Pa ana a Kisi panali Yerameeli. 30 Ndipo ana a Musi anali Mali, Ederi ndi Yerimoti.
Amenewa anali ana a Levi potsatira nyumba za makolo awo. 31 Iwonso anachita maere+ ngati mmene abale awo, ana a Aroni, anachitira pamaso pa Mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki ndiponso atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi. Nyumba ya makolo ya wamkulu inali chimodzimodzi ndi nyumba ya makolo ya wamngʼono.