1 Samueli
13 Sauli anali ndi zaka . . .* pamene anakhala mfumu,+ ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 2 Sauli anasankha amuna 3,000 a mu Isiraeli. Pa amunawa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi komanso kudera lamapiri la Beteli. Pamene amuna 1,000 anali ndi Yonatani+ ku Gibeya+ wa ku Benjamini. Anthu ena onse otsalawo anawauza kuti abwerere kumatenti awo. 3 Kenako Yonatani anapha asilikali a Afilisiti+ amene anali ku Geba+ ndipo Afilisiti anamva zimenezi. Zitatero Sauli analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ mʼdziko lonse nʼkunena kuti: “Tamverani Aheberi nonse!” 4 Aisiraeli onse anamva nkhani yakuti: “Sauli wapha asilikali a Afilisiti moti panopa Aisiraeli akhala chinthu chonunkha kwa Afilisiti.” Choncho anasonkhanitsa anthu onse kuti atsatire Sauli ku Giligala.+
5 Nawonso Afilisiti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisiraeli. Iwo anali ndi magaleta ankhondo 30,000, asilikali okwera pamahatchi 6,000 ndi asilikali oyenda pansi ambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+ Kenako anapita ku Mikimasi nʼkumanga msasa kumʼmawa kwa Beti-aveni.+ 6 Ndipo amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zavuta chifukwa anapanikizika kwambiri. Anthu anakabisala mʼmapanga,+ mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼzipinda zapansi ndi mʼzitsime zopanda madzi. 7 Aheberi ena mpaka anawoloka Yorodano nʼkupita mʼdera la Gadi ndi Giliyadi.+ Koma Sauli anali adakali ku Giligala ndipo anthu onse amene ankamutsatira ankanjenjemera. 8 Sauli anapitiriza kudikira kwa masiku 7 mpaka nthawi imene anagwirizana ndi Samueli. Koma Samueli sanafikebe ku Giligala ndipo anthu anayamba kubalalika kumusiya Sauli. 9 Kenako Sauli anati: “Bweretsani nsembe yopsereza ndi nsembe zamgwirizano.” Ndipo iye anapereka nsembe yopsereza.+
10 Koma atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, Samueli anafika. Choncho Sauli anapita kukamulandira ndipo anamudalitsa. 11 Ndiyeno Samueli anati: “Ndiye chiyani wachitachi?” Sauli anayankha kuti: “Ndinaona kuti anthu akubalalika kundisiya ndekha,+ ndipo inu simunabwere pa nthawi imene tinagwirizana ija. Ndinaonanso kuti Afilisiti akusonkhana ku Mikimasi.+ 12 Ndiye ndinaganiza kuti, ‘Afilisitiwa abwera ku Giligala kuno kudzamenyana nane, ndipo sindinakhazike pansi mtima wa Yehova.’ Choncho ndinaona kuti ndiyenera kupereka nsembe yopsereza.”
13 Koma Samueli anauza Sauli kuti: “Zimene wachitazi ndi zopusa. Sunamvere lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.+ Ukanamvera, Yehova akanachititsa kuti banja lako lilamulire Isiraeli mpaka kalekale. 14 Koma tsopano ufumu wako sukhalitsa.+ Yehova apeza munthu wapamtima pake,+ ndipo Yehova amuika kukhala mtsogoleri wa anthu ake+ chifukwa iwe sunamvere zimene Yehova anakulamula.”+
15 Kenako Samueli ananyamuka kuchoka ku Giligala kupita ku Gibeya wa ku Benjamini. Ndiyeno Sauli anawerenga anthu nʼkupeza kuti amene anatsala naye analipo amuna pafupifupi 600.+ 16 Sauli, mwana wake Yonatani komanso anthu amene anatsala nawo aja ankakhala ku Geba+ wa ku Benjamini. Koma Afilisiti anali atamanga msasa ku Mikimasi.+ 17 Magulu atatu a asilikali ankabwera kuchokera mumsasa wa Afilisiti nʼkumalanda katundu. Gulu loyamba linkalowera kumsewu wopita ku Ofira, kudera la Suwali. 18 Gulu lachiwiri linkalowera kumsewu wa ku Beti-horoni,+ ndipo gulu lachitatu linkalowera kumsewu wopita kumalire oyangʼanizana ndi chigwa cha Zeboyimu, molunjika kuchipululu.
19 Mʼdziko lonse la Isiraeli munalibe wosula zitsulo. Izi zinali choncho chifukwa Afilisiti anati: “Kuti Aheberi asasule lupanga kapena mkondo.” 20 Choncho Aisiraeli onse akafuna kunola pulawo, khasu, nkhwangwa kapena chikwakwa, ankapita kwa Afilisiti kuti akawanolere. 21 Ndipo malipiro onoletsera mapulawo, makasu, mafoloko a mano atatu ndi nkhwangwa, ndiponso kukonza chisonga chotosera ngʼombe anali pimu* imodzi. 22 Ndipo pa tsiku lankhondo, pa anthu onse amene anali ndi Sauli ndi Yonatani panalibe aliyense amene anali ndi lupanga kapena mkondo.+ Sauli yekha ndi mwana wake Yonatani ndi amene anali ndi zida.
23 Gulu la asilikali a Afilisiti linachoka kumsasa kupita kumalo owolokera a ku Mikimasi.+