Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 tsamba 1945-1947
  • 8 Kukhalapo kwa Khristu (Pa·rou·siʹa)

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 8 Kukhalapo kwa Khristu (Pa·rou·siʹa)
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
8 Kukhalapo kwa Khristu (Pa·rou·siʹa)

8 Kukhalapo kwa Khristu (Pa·rou·siʹa)

Mt 24:3—Chigiriki, τὸ σημεῖον τῆς σῆς παρουσίας (to se·meiʹon tes ses pa·rou·siʹas)

1864

“CHIZINDIKIRO cha kukhalapo KWANU”

The Emphatic Diaglott (J21), lomasuliridwa ndi Benjamin Wilson, New York ndi London.

1897

“chizindikiro cha kukhalapo kwanu”

The Emphasised Bible, lomasuliridwa ndi J. B. Rotherham, Cincinnati.

1903

“chozindikiritsa kukhalapo Kwanu”

The Holy Bible in Modern English, lomasuliridwa ndi F. Fenton, London.

1950

“chizindikiro cha kukhalapo kwanu”

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, Brooklyn.

Tanthauzo lenileni la mawu achigiriki akuti pa·rou·siʹa, ndi lakuti “kukhala pambali pa.” Mawuwa ndi otengedwa ku mawu osonyeza malo akuti pa·raʹ (pambali pa) ndi mawu akuti ou·siʹa (“kukhala”). Mawu akuti pa·rou·siʹa amapezeka m’malo okwanira 24 m’Malemba Achigiriki. Malowo ndi awa: Mt 24:3, 27, 37, 39; 1Ak 15:23; 16:17; 2Ak 7:6, 7; 10:10; Afi 1:26; 2:12; 1At 2:19; 3:13; 4:15; 5:23; 2At 2:1, 8, 9; Yak 5:7, 8; 2Pe 1:16; 3:4, 12 ndi 1Yo 2:28. M’malo 24 amenewa, Baibulo la Dziko Latsopano lamasulira pa·rou·siʹa kuti “kukhalapo,” ndi mawu ena ofanana ndi amenewa.

Mneni wa mawuwa wakuti paʹrei·mi, kwenikweni amatanthauza “khala pambali pa.” Akupezeka maulendo 24 m’Malemba Achigiriki m’malo awa: Mt 26:50; Lu 13:1; Yoh 7:6; 11:28; Mac 10:21, 33; 12:20; 17:6; 24:19; 1Ak 5:3, 3; 2Ak 10:2, 11; 11:9; 13:2, 10; Aga 4:18, 20; Akl 1:6; Ahe 12:11; 13:5; 2Pe 1:9, 12 ndi Chv 17:8. M’malo amenewa, Baibulo la Dziko Latsopano lamasulira paʹrei·mi m’njira zosiyanasiyana koma ndi tanthauzo la “kukhalapo.”

Tikaona mmene akusiyanitsira kukhalapo ndi kusakhalapo kwa Paulo pa 2Ak 10:10, 11 komanso pa Afi 2:12, tanthauzo la pa·rou·siʹa likuonekeratu. Komanso, tikaona mmene akuyerekezera pa·rou·siʹa ya Mwana wa munthu ndi “masiku a Nowa” pa Mt 24:37-39, zikuonekeratu kuti mawu amenewa amatanthauza “kukhalapo.”

Mtanthauzira mawu wolembedwa ndi Liddell ndi Scott pofotokoza matanthauzo a mawu akuti pa·rou·siʹa, anaika mawu akuti kukhalapo monga tanthauzo loyamba la mawuwa. (A Greek-English Lexicon (LSJ), tsa. 1343) Mofanana ndi zimenezi, mtanthauzira mawu wotchedwa TDNT, Vol. V, tsa. 859, pakamutu kakuti “Tanthauzo Lake Lalikulu” amati: “παρουσία [pa·rou·siʹa] kwenikweni amatanthauza kukhalapo, n’kumachita zinazake.”

Liwu lakuti pa·rou·siʹa, “kukhalapo,” ndi losiyana ndi liwu lachigiriki lakuti eʹleu·sis, “kubwera,” limene limapezeka kamodzi kokha m’Malemba Achigiriki, pa Mac 7:52, monga e·leuʹse·os (Chilatini, ad·venʹtu). Mawu akuti pa·rou·siʹa ndi eʹleu·sis sagwiritsidwa ntchito ngati mawu ofanana. Mtanthauzira mawu wotchedwa TDNT, Vol. V, tsa. 865, anati “mawuwa [paʹrei·mi ndi pa·rou·siʹa] sagwiritsidwa ntchito ponena za kubwera kwa Khristu ndi thupi la nyama, ndipo παρουσία [pa·rou·siʹa] alibe n’komwe tanthauzo la kubweranso. Maganizo akuti palinso pa·rou·siʹa wina anayambira m’tchalitchi m’zaka za m’ma 100 C.E. [Maganizo amenewa anayamba Justin wa m’zaka za m’ma 100 C.E., atakhalapo kale.] . . . Kuti timvetse mmene Akhristu oyambirira ankaganizira, choyamba tiyenera kuchotseratu m’maganizo mwathu maganizo amenewo [akuti palinso pa·rou·siʹa wina].”

Ponena za tanthauzo la mawu amenewa, Israel P. Warren, D.D., m’buku lake analemba kuti: “Kawirikawiri ifeyo timanena za ‘kubweranso kwachiwiri,’ ndi mawu ena otero, koma Malemba sanenapo chilichonse za ‘pa·rou·siʹa wachiwiri.’ Mulimonse mmene zikanakhalira, pa·rou·siʹa anayenera kukhala chochitika chachilendo. Anayenera kukhala chinthu chimene sichinachitikepo ndi kale lonse, ndiponso choti sichidzachitikanso. Anayenera kukhala ‘kukhalapo’ kwake kosiyana kwambiri ndiponso kwapamwamba kwambiri kuposa nthawi zonse zimene iye anaonekerapo kwa anthu. N’chifukwa chake mawu akuti KUKHALAPO, ayenera kuima pawokha, osawonjezerapo mawu ena.

“Tikaona mawu akuti ‘pa·rou·siʹa’ mwa njira imeneyi, ndikuona kuti zikuchita kuonekeratu kuti mawu akuti ‘kubwera’ sakuimira bwino mawu oyambirira amene anagwiritsidwa ntchito. Sakugwirizana ndi mmene mawu akuti pa·rou·siʹa anayambira. Sakugwirizananso ndi mfundo yaikulu ya mneni amene mawu amenewa anachokerako. Komanso, sangagwiritsidwe ntchito bwinobwino kuti alowe m’malo mwa mawu amene amamasulira bwino kwambiri pa·rou·siʹa, akuti ‘kukhalapo’ m’malo amene omasulira anagwiritsira ntchito mawu akuti ‘kukhalapo’ amenewa. Komanso, mfundo yaikulu ya mawu akuti ‘kubwera’ ndi yosiyana ndi mfundo yaikulu ya pa·rou·siʹa. Mawu akuti ‘kubwera’ akutsindika kwambiri mfundo ya kutiyandikira, kuyenda n’kumalowera kumene ife tili. Koma mawu akuti ‘pa·rou·siʹa’ ali ndi mfundo ya kukhala nafe, popanda kutchula momwe zachitikira kuti akhale nafe. ‘Kubwera’ kumatha chinthucho chikafika. Koma ‘kukhalapo’ kumayamba chinthucho chikafika. Mawu akuti ‘kubwera’ akusonyeza kuti chinthucho chikuyenda, pamene akuti ‘kukhalapo’ akusonyeza kuti chinthucho sichikuyendanso. Nthawi imene chinthu chimakhala ‘chikubwera’ ndi yochepa, mwinanso ikhoza kungokhala kanthawi kochepa kwambiri, koma nthawi imene chinthu ‘chimakhalapo’ ilibe malire . . . .

“Pomasulira mawu akuti ‘pa·rou·siʹa’ zikanakhala bwino omasulira athu akanachita zimene anachita ndi mawu akuti ‘baptisma.’ Mawu akuti ‘baptisma’ anangowasamutsira ku chinenero china osawasintha. Kapena, zikanakhala bwino akanamasulira mawu akuti ‘pa·rou·siʹa’ pogwiritsira ntchito mawu akuti kukhalapo, amene ndi ofanana nawo kwambiri malinga ndi mmene mawuwo anayambira. Zikanatero, anthu akanamvetsetsa kuti palibe chinthu chotchedwa ‘Kukhalapo kwachiwiri,’ ndipo ndikukhulupirira kuti chiphunzitso chonsechi chikanakhala chosiyana ndi mmene chilili panopa. Mawu akuti ‘kubweranso kwachiwiri’ sakanamvedwapo n’komwe. Anthu opita kutchalitchi akanaphunzitsidwa kuti KUKHALAPO KWA AMBUYE n’kumene kudzakwaniritse zinthu zimene akuziyembekezera, kaya posachedwapa kapena pa nthawi inayake yapatali kwambiri kutsogoloku. Akanaphunzitsidwanso kuti kukhalapo kwa Ambuye n’kumene kudzachititse kuti dziko likhalenso latsopano, kuti anthu aukitsidwe mwakuthupi ndiponso mwauzimu, ndiponso kuti chilungamo ndi mphoto zamuyaya ziperekedwe.”—The Parousia, Portland, Maine (1879), masamba 12-15.

Komanso, mtanthauzira mawu wolembedwa ndi Bauer, patsamba 630, amanena kuti mawu akuti pa·rou·siʹa “anakhala mawu amene akuluakulu a boma anali kugwiritsa ntchito akamafotokoza za ulendo wa anthu olemekezeka, makamaka mafumu ndi akazembe amene abwera kudzayendera chigawo cha dziko.” Pa Mt 24:3, komanso m’malemba ena monga 1At 3:13 ndi 2At 2:1, mawu akuti pa·rou·siʹa akunena za kukhalapo kwa Yesu Khristu monga Mfumu, kuchokera pamene analongedwa ufumuwo m’masiku otsiriza a nthawi ino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena