10 Yesu, Wonga Mulungu; Waumulungu
Yoh 1:1—“komanso Mawuyo anali mulungu (wonga Mulungu; waumulungu)”
Chigiriki, καὶ θεὸς ἦν ὁ λόγος (kai the·osʹ en ho loʹgos)
1808 |
|
The New Testament, in An Improved Version, Upon the Basis of Archbishop Newcome’s New Translation: With a Corrected Text, London. |
1864 |
|
The Emphatic Diaglott (J21, kuwerenga motsatira Chigiriki), lomasuliridwa ndi Benjamin Wilson, New York ndi London. |
1879 |
|
La Sainte Bible, Segond-Oltramare, Geneva ndi Paris. |
1928 |
|
La Bible du Centenaire, Société Biblique de Paris. |
1935 |
|
The Bible—An American Translation, lomasuliridwa ndi J. M. P. Smith ndi E. J. Goodspeed, Chicago. |
1950 |
|
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, Brooklyn. |
1975 |
|
Das Evangelium nach Johannes, lomasuliridwa ndi Siegfried Schulz, Göttingen, Germany. |
1978 |
|
Das Evangelium nach Johannes, lomasuliridwa ndi Johannes Schneider, Berlin. |
1979 |
|
Das Evangelium nach Johannes, lomasuliridwa ndi Jürgen Becker, Würzburg, Germany. |
Mabaibulo amenewa a Chingelezi, Chifalansa, ndi Chijeremani, amagwiritsa ntchito mawu akuti “mulungu,” “waumulungu” kapena “wonga Mulungu,” chifukwa chakuti mawu achigiriki akuti the·osʹ (θεός) analembedwa opanda mawu akuti ho. Koma pamawu akuti “ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu,” “Mulungu” amene Mawuyo, kapena Logosi, anali naye pa chiyambipo, akutchulidwa pano ndi mawu achigiriki akuti ὁ θεός, kutanthauza the·osʹ wokhala ndi ho. M’Chigiriki choyambirira, kalembedwe kotere kamasonyeza kuti munthuyo ndani, pamene the·osʹ wopanda ho amasonyeza khalidwe la munthuyo. Choncho, mawu a Yohane akuti Mawuyo, kapena Logosi, anali “mulungu,” kapena “waumulungu,” kapenanso “wonga Mulungu,” sakutanthauza kuti iye anali Mulungu weniweniyo amene iye anali naye. Amangosonyeza khalidwe la Mawuyo, kapena Logosi, koma sakunena kuti iyeyo ndiye Mulungu weniweniyo. N’chifukwa chake, pa Yoh 1:1 mu Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, tinalemba “mulungu” wa “m” wamng’ono m’mawu akuti “komanso Mawuyo anali mulungu,” pofuna kum’siyanitsa ndi Mulungu weniweniyo amene nthawi zonse timamulemba ndi “M” wamkulu.
a Lomasuliridwa kuchokera ku Chifalansa.
b Lomasuliridwa kuchokera ku Chifalansa.
c Lomasuliridwa kuchokera ku Chijeremani.
d Lomasuliridwa kuchokera ku Chijeremani.
e Lomasuliridwa kuchokera ku Chijeremani.