Tsamba 2
Pamene anali pa kuweruzidwa pamaso pa wolamulira Wachiroma Pontiyo Pilato, Yesu Kristu ananena kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.”—Yohane 18:36.
Kodi akulu ansembe ali ndi kawonedweka lerolino? Kodi chiri chothekera m’nthaŵi yathu kukhala m’dziko ndipo kusakhalabe mbali ya ilo? Kodi ndi mbali yotani ya chipembedzo m’ndale zadziko zamakono?