Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 5/8 tsamba 32
  • Kuchita ndi Malingaliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita ndi Malingaliro
  • Galamukani!—1988
Galamukani!—1988
g88 5/8 tsamba 32

Kuchita ndi Malingaliro

Kuchita tero mwachipambano chiri chitokoso chenicheni. Wachichepere akulongosola chokumana nacho chake: “Ndinkadzimva wachimwemwe, koma mphindi yotsatira ndinali m’kupsyinjika kozama. Nthaŵi zina sindinakhoze ngakhale kudziŵa chomwe ndinkalingalira. Kunali monga ngati kuti ndinali wotaika kotheratu m’mdima. Sindikanatha kudzilongosola inemwini ndi chimene malingaliro anga anali mosasamala kanthu kuti ndi kwayani komwe ndinalankhula, osati ngakhale kwa inemwini. Ndinkadzimva monga ngati kuti sindinali kupeza chisamaliro kuchokera kwa anthu ondizinga ine, makamaka anzanga a ku sukulu, chifukwa chakuti sindinali kokha wokwanira. Potsirizira pake malingaliro onsewa ankandipha ine mkati, ndipo ndinayamba kudzida inemwini ndi umunthu wanga.”

Mtsikanayu anali ndi kope la bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It. “Ilo linali lokondweretsa kwenikweni,” iye akulemba tero, “chotero ndinafuna kuŵerenga mutu wotsatira, womwe uli wakuti ‘Kufika Kuukazi.’ Sindinakhulupirire zomwe ndinkaŵerenga. Mutuwo unalongosola ndendende momwe ndinkadzimverera papitapo, kuphatikizapo ndi yankho. Chinali cholimbikitsa koposa kuŵerenga kuti chinali molondola cha nthaŵi zonse kudzimva mwanjirayi. Ndimangofunikira kudziŵa njira yolondola ya kuchita nazo.”

Pambali pa kuthandiza achichepere kuchita ndi malingaliro awo, bukhu limeneli limakambitsirana nkhani zonga ngati kuchita phyotophyoto ndi kuyankha mafunso akuti, Kodi achichepere ayenera kumwa zakumwa zoledzeretsa ndipo, Kodi ayenera kugonana asanakwatirane? Landirani kope pa K8.00 yokha mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Your Youth—Getting the Best out of It. Ndatsekeramo K8.00 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena