Dzanja—‘Chiwalo Chaluso Chokongola Koposa’
INALI ngozi. Mtsikana wachichepere analigone pa khomo la chipatala, mtsempha waukulu wa mwazi m’mwendo wake wakulamanja utavulazika pa ngozi ya pa njinga yamoto. Panalibe ziwiya zimene zinalipo kuti aletse kutuluka kwa mwazi pa chirondapo. Kodi nchiyani chimene dokotala akanachita?
“Ndinagwiritsira ntchito dzanja langa monga chosindikiza,” akukumbukira tero Profesa Napier m’bukhu lake Hands, “ndikumasindikiza mtsempha waukulu wa mwaziwo ndi chala chamanthu ndi chala cholozera kulingana ndi mmene ndinathera. Potsirizira pake ndinapeza nthambo yaing’ono, chonse chomwe chinalipo, ndinaizungulitsa ku mtsempha waukulu wa mwaziwo ndi kuwumanga iwo. Mwazi unaleka kutuluka. . . . Palibe china chirichonse koma manja akanakhoza kuchita ndi ngozi imeneyo mofulumira ndipo mokhutiritsa. Odwala oŵerengeka . . . amazindikira kuti ndimotani, mkati mwa kutumbula, chala choikidwa pa malo abwino chinapulumutsira miyoyo yawo.”
Machitidwe onga awa akanakhala osatheka ngati panalibe kulumikizidwa kokhoza kukhota kwa chala chamanthu. (Onani chitsanzo.) Kalinganizidwe kake kamalola chifupifupi kusamukasamuka kochulukira konga ngati kulumikizidwa kwa fupa longa mpira la phewa, koma mosiyana ndi limeneli, kulumikizidwako sikumafunikira kuchirikiza kuchokera ku unyinji wa minofu yoizungulira. Chala chamanthu, ngakhale ndi tero, chingapange kuyendayenda kovuta pamene chikumana ndi nsonga za zala.
Yesani kunyamula chinthu chaching’ono ngakhale kutembenuza tsamba la magazini ino popanda kugwiritsira ntchito chala chanu chamanthu. Anatero dokotala wa ku South Africa: “Ndaika zala zamanthu zovulazika zochulukira zomangidwa ndi mitengo, ndipo pamene odwalawo abweranso, iwo kaŵirikaŵiri amandiwuza ine kuti sanazindikire mmene anafunira zala zawo zamanthu.”
Dzanja la munthu ndi chala chake cha pambali chamanthu liri mozizwitsa chiwiya chosinthasintha. Popanda dzanja, ndimotani mmene mukalembera kalata, kujambula chithunzithunzi, kukhoma msomali, kugwiritsira ntchito lamya, kapena kuika ulusi ku singano? Tiyamikira dzanja, woliza piyano amaseŵera nyimbo zosangalatsa kwenikweni, a luso la manja amapaka utoto ku zithunzithunzi zokongola, ndipo adokotala amapanga kutumbula kovuta kwenikweni. “Anyani, okhala ndi zala zamanthu zazifupi ndi zala zazitali, amasowa chochita m’chigwirizano ndi ntchito yovuta yofunikira luso ya manja,” yalongosola tero The New Encyclopædia Britannica.
Pali kusiyana kwina kofunika pakati pa dzanja la munthu ndi lija la nyani. Chifupifupi gawo limodzi mwa anayi a gawo lochita ndi uthenga (motor cortex) mu ubongo wa munthu liri loperekedwa ku mphamvu za manja anu. Gawo lochita ndi uthenga la munthu, yalongosola tero Textbook of Medical Physiology ya Profesa Guyton, “liri losiyana kwenikweni ndi lija la nyama wamba” ndipo limapanga kuthekera “kwa kukhoza kwapadera kwa kugwiritsira ntchito dzanja, zala, ndi chala chamanthu kuchita ntchito yaluso kwenikweni ya manja.”
M’kuwonjezerapo, adokotala a minyewa ya mu ubongo apeza gawo lina la ubongo wa munthu lomwe amalitcha “mbali ya maluso a dzanja.” Manja a luso afunikira mitsempha yolandirira zizindikiro. Mbali zothera zazing’ono za mitsempha zimenezi ziri zambiri mu dzanja la munthu, makamaka mu chala chamanthu. Dokotala yemwe anafunsidwa ndi Galamukani! ananena kuti: “Pamene anthu ataikiridwa ngakhale kuzindikira kochepera kwa nsonga ya chala chawo chamanthu, amachipeza icho kukhala chovuta kukhazikitsa zinthu zazing’ono zonga ngati misomali ya mazinga.” Mikono yanu iri ndi mtundu wina wa mitsempha yolandirira zizindikiro imene imakutheketsani kusinthira dzanja lanu ku malo olondola ngakhale mu mdima wa ndiwe yani. Chotero, pamene muligone pa kama usiku, mungakhoze kukanda mphuno yanu popanda kukantha pa maso.
Ngakhale kachitidwe kopepuka konga ngati kufikira chikho cha madzi kali kenakake kozizwitsidwa nako. Ngati kugwira kwanu kuli kofooka, mungagwetse chikhocho. Ngati kugwira kwanu kuli kwamphamvu kwambiri, mungachiswe icho, ndi kuvulaza zala zanu. Kodi ndimotani mmene mumakhozera kuchigwira icho kokha ndi mphamvu zolondola? Mitsempha yolandirira mphamvu m’dzanja lanu imatumiza uthenga ku ubongo wanu, umene umabwezanso malangizo olondola ku minofu mumkono wanu wotambasulidwawo ndi dzanja.
Mwamsanga, popanda kuyang’ana kwanu, chikhocho chimadzakhala bwino lomwe pakati pa milomo yanu. Pa nthaŵiyo, chisamaliro chanu chingakhale choperekedwa pa programu ya wailesi ya kanema kapena kukambitsirana ndi mabwenzi. “Chenicheni chakuti chikho chimaperekedwa kukamwa popanda kugundidwa pamaso,” walongosola tero Dr. Miller m’bukhu lake The Body in Question, “chiri ulemelero ku mphamvu zolinganiza zodabwitsa za mkono wotambatsulidwa. Ndipo chenicheni chakuti chikhocho chimakhalabe pakamwa pamene chikutha kulemelera m’nthaŵi imene icho chikutsirizidwa madzi chimasonyeza kufulumira kumene uthengawo umatumizidwanso.”
Nchosadabwitsa kuti dzanja la munthu lapangitsa anthu olingalira kuzizwitsidwa! “Popanda chitsimikiziro china chirichonse,” analemba tero wasayansi wotchuka Sir Isaac Newton, “chala chamanthu chokha chikhoza kundikhutiritsa ine za kukhalapo kwa Mulungu.” “Tingapereke anthu ku mwezi,” wanena tero Profesa Napier, “koma, kwa zopangapanga zathu zonse za umakanika ndi magetsi zozizwitsa, sitingakhoze kupanganso chala cholozera choyerekezera chomwe chingakhoze kumva limodzinso ndi kukodola.” Dzanja la munthu, yalongosola tero The New Encyclopædia Britannica, liri mwinamwake “chiwalo cha zolengedwa chaluso kopambana” ndipo chimodzi chimene “chimamusiyanitsa iye kuchoka ku zamoyo zina zonse.”
[Zithunzi patsamba 5]
Kulumikizidwa kosinthasintha kwa chala chamanthu kuli kwapadera kutalinganizidwa ndi kulumikizidwa kwina kwa zala zina
[Zithunzi patsamba 6]
Dzanja la munthu ndi chala chake chapambali chamanthu liri mozizwitsa chiwiya chokhoza kusintha
[Chithunzi patsamba 6]
Mitsempha yolandirira zizindikiro m’dzanja lanu ndi mkono imatheketsa ubongo wanu kulinganiza kachitidwe kocholowanacholowana