Tsamba 2
Ndi kugwa kwa mabanja ndi mikhalidwe yonyonyotsoka m’masukulu, achichepere avutika. Ngakhale mfuti, mipeni, ndi anamgoneka zakhala zofala m’masukulu a mizinda yaikulu. Kodi nchiyani chimene chiri mathayo ochepera a masukulu ndi makolo m’kuphunzitsa ndi kulera ana? Kodi nchiyani chimene achichepere amafunikira kwenikweni kuchokera kwa makolo awo? Kodi ndi ntchito ya kunyumba yotani imene makolo ayenera kuchita ngati ana awo ati akhale achikulire achipambano?
Chiwopsyezo cha kuwonongedwa kotheratu kwa nyukliya chawopsyeza mtundu wa anthu kwa zaka zoposa makumi anayi. Kuyambitsidwa kwa posachedwapa kwa mtendere, ngakhale kuli tero, kwadzetsa ziyembekezo kaamba ka kuleka kugwiritsiridwa ntchito kotheratu kwa zida. Kodi ziyembekezo zoterozo ziri zenizeni motani? Galamukani! tsopano ikuyang’ana pa nsonga zocholowanacholowana zozungulira nkhani ya kusagwiritsira ntchito zida za nyukliya.