Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 5/8 tsamba 32
  • Chiwawa—Mapeto Akuwonekera!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiwawa—Mapeto Akuwonekera!
  • Galamukani!—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?
    Galamukani!—2002
  • Kutheratu kwa Chiwawa—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chiwawa
    Galamukani!—2015
  • Padziko Lonse Pakuchitika Zachiwawa Zokhudza Ndale—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 5/8 tsamba 32

Chiwawa—Mapeto Akuwonekera!

ANTHU akhala ndi nthaŵi yochulukira ya kuika chiwawa pansi pa ulamuliro, koma icho changokula moipirako. Kodi icho sichiri chodziŵikiratu kuti anthu sangathe kuchichita? Ndi chiyembekezo chotani, kenaka, chomwe chiripo kaamba ka mapeto a chiwawa?

Motsimikizirika, ndi kwa Mlengi wawo kumene anthu afunikira kuyang’ana kaamba ka chothetsera ku vutolo, limodzinso ndi mavuto ena onse. Yankho lake liri Ufumu wake, womwe uli boma lakumwamba lolungama. Yesu Kristu anapereka ntchito yake yolalikira pa dziko lapansi kuwuza anthu ponena za boma la Ufumu limenelo. Mumapemphera kaamba ka boma limeneli pamene mumanena kuti: “Ufumu wanu udze. Chifuniro chanu chichitike m’dziko lapansi, monga mmene ziriri kumwamba.”—Mateyu 6:9, 10, King James Version.

Koma kodi ndimotani mmene Ufumu wa Mulungu udzathetsera chiwawa? Poneneratu masiku enieni mu amene tikukhala, Baibulo limanena kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Inde, boma la Ufumu wa Mulungu lidzawononga kotheratu maboma amakono a dziko lapansi ndi zitaganya zomwe iwo akulamulira, zokhala ndi chiwawa chawo chonse ndi upandu.

Koma kodi ndi liti pamene ichi chidzachitika? Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti kudzakhala m’nthaŵi yathu. Nchifukwa ninji tikunena chimenechi? Chifukwa chakuti “chizindikiro” chimene Yesu ananena kuti chidzazindikiritsa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” tsopano chikukwaniritsidwa. “Chizindikiro” chimenechi chimaphatikizapo “kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:3-14, 34) Ndi mpumulo wozizwitsa chotani nanga pamene Mulungu adzachotsapo dziko lodzala ndi chiwawa iri! Ngakhale kuli tero, kuti tikasangalale ndi madalitso nthaŵiyo, tiyenera kuchita chifuniro cha Mulungu tsopano.—1 Yohane 2:17.

Ulosi wa Baibulo wolembedwa ndi mneneri wakale Yesaya umanena za kuitana kwa Mulungu kugonjera ku malangizo Ake ndi “kuyenda m’mayendedwe ake.” Awo omwe omavomereza, ulosiwo ukunena kuti, “adzasula malupanga awo akhale zolimira” ndipo “sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:3, 4) Ulosi wina wolembedwa ndi Yesaya umanena za chotulukapo: “Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m’malire ako.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “Yehova adzakhala kwa iwe kuwunika kosatha.”—Yesaya 60:18-20.

Ngakhale kuti mlingo wa mtendere ungasangalalidwe ngakhale tsopano mwa kuphunzira chifuniro cha Yehova Mulungu ndi kugonjera ku icho, tangolingalirani mmene chidzakhalira posachedwapa pamene Ufumu wa Mulungu udzachotsa m’dziko lapansi chisalungamo chonse. Kenaka sipadzakhala chochititsa mantha, sipadzakhala chifukwa cha kuwopera kuyenda m’khwalala lirilonse kapena kuloŵa mu parki iriyonse usiku. Sipadzakhala kufunika kulikonse kwa maloko pa zitseko zanu, sipadzakhala kufunika kwa kudera nkhaŵa ponena za kudzichinjiriza inu eni.—2 Petro 3:13.

Kodi mungakonde kukhala m’dziko latsopano lotero lomasuka ku chiwawa? Ichi chingakhale chiyembekezo chanu cha chimwemwe, popeza kuti chazikidwa pa Mawu otsimikizirika a Mlengi wathu iyemwini. Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kukuthandizani kumvetsetsa ziyembekezo zabwino zimenezi zimene Mlengi wathu akufutukula kwa tonsefe. Bwanji osapanga kudziyambira kufufuza inu eni? Inu nanunso mungasangalale, mukumadziŵa kuti chiwawa chidzatha—posachedwapa!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena