Tsamba 2
“Nduna za ku Latin America tsopano zikuchenjeza kuti m’dziko limodzi pambuyo pa linzake, kugwa kwa miyezo ya kakhalidwe kukuyambitsa kupanda chiyembekezo komwe kukuyamba kusinthira ku kugwa kowopsya kwa ndale zadziko.”—The New York Times, November 29, 1988.
Mkati mwa ma 1980, mamiliyoni a anthu—omwe anali kale osauka mosowa chochita—awona kukwera kwa mtengo wa zinthu kukutsiriza ndalama zawo zochepa zomwe amapezazo ngakhale mopitirira. Kwa iwo, siliri kokha funso la kuchita ndi mtengo wa kakhalidwe koma, m’malomwake, nkhani ya kulimbana kuti afikiritse mtengo wa chipulumuko. Kodi mwawona kukwera mitengo kwa zakudya zofunikira m’dziko lanu? Kodi icho chikuwoneka ngati kuti thumba lanu la zinthu zogula likucheperachepera kaamba ka unyinji wa ndalama zimene mumawononga? Kenaka, mofanana ndi anthu ena ambiri, mukudziŵa kuchokera ku chokumana nacho kuti mtengo wa kakhalidwe ukuwonjezereka.
Kodi pali yankho?