Kuyendayenda mu Imfa
Pamene kuli kwakuti dziko likuwononga chifupifupi madola triliyoni imodzi pa chaka kaamba ka zida zankhondo:
Anthu 800,000,000 akukhala mu umphaŵi wotheratu
770,000,000 alibe chakudya chokwanira kaamba ka moyo wogwira ntchito mokangalika
100,000,000 alibe pogona
1,300,000,000 alibe madzi akumwa achisungiko
Ana 14,000,000 amafa chaka chirichonse chifukwa cha ziyambukiro za njala
IWO atchedwa Amalonda a Imfa, Okumba Manda a Kutsungula, Kansa Yotupa pa Thupi la Chitaganya. Ndani? Amalonda a zida zankhondo a dziko. Chifukwa ninji?
Mu nthaŵi zakale, iwo anasunga magulu ankhondo okonzekeretsedwa ndi malupanga, mikondo, nkhwangwa, ndi mivi kaamba ka kupha kwa munthu ndi munthu pa mabwalo ankhondo. M’zana lino, iwo anapanga ndi kugawira mfuti, mabomba, akasinja, zombo zankhondo, ndege, gas ya ululu, ndi zipolopolo zophera makumi a mamiliyoni a anthu mu nkhondo zadziko ziŵiri pamene panthaŵi imodzimodziyo akuwononga mabiliyoni a madola a magwero a chuma, onga ngati mizinda, nyumba, ndi katundu wina. Iwo anapangitsa nkhondo zoposa 120 zomenyedwa chiyambire mapeto a Nkhondo ya Dziko ya II.
Iwo akupitirizabe kupangitsa nkhondo zokhetsa mwazi mu mbali zosiyanasiyana za dziko. Iwo amaphunzitsa magulu ankhondo a Maiko Otukuka Kumene kaamba ka kugwiritsira ntchito kokhutiritsa kwa zida zawo. Iwo akonzekeretsa mphamvu zankhondo za dziko ndi mulu wa zida za nyukliya zokhoza kuphulitsa banja la anthu nthaŵi zingapo mobwerezabwereza ndi kusintha dziko lapansi kukhala pulaneti losakhalidwamo. Iwo akuwoneka kukhala osasamala kotheratu. Liwu lawo la kunyada lingakhale lakuti: “Imfa yanu—phindu lathu.”
Palibe malonda amene ayambukira banja la anthu mwakuya chotero monga malonda a zida zankhondo. Maumboni ali owonekera bwino. Nkhani yotsatira idzavumbula nsonga zina zovutitsa maganizo.