Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 11/8 tsamba 32
  • Kodi Nkuwaphonyeranji Iwo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkuwaphonyeranji Iwo?
  • Galamukani!—1989
Galamukani!—1989
g89 11/8 tsamba 32

Kodi Nkuwaphonyeranji Iwo?

Pamene anali m’mzera pa banki ya mu Mzinda wa New York, mkazi wa zaka zapakati anawona mwamuna wina patsogolo pake akuŵerenga magazine a The Watchtower (Nsanja ya Olonda). Mkaziyo anali wofunitsitsa kuŵerengamo nkhani yonena za pemphero, chotero anasunga deti la kopelo.

Masiku oŵerengeka pambuyo pake, Mboni za Yehova zinafika pa khomo pake, ndipo iye anafunsa nati: “Kodi muli nawo makope a July a The Watchtower (Nsanja ya Olonda)?” Atadziŵa chifukwa chimene mkaziyo anali wokondweretsedwa m’magazine amodzi okhawo, mmodzi wa Mbonizo anamdziŵitsa iye kuti: “Njira yabwino ya kusaphonya makope aliwonse osangalatsa ndiyo kulembetsa.”

“Sindinadziŵe kuti wina angatero!” anafuula tero mkaziyo. Pamene anawuzidwa kuti sabusikripishoni ya chaka chimodzi inali $5 (K80) yokha, anayankha nati: “Kodi munena zowona? [K80] yokha kwa chaka chathunthu?” Pamene anatsimikiziridwa kuti zinalidi tero, iye sanangofuna The Watchtower (Nsanja ya Olonda) yokha komanso ndi magazine anzake, Awake! (Galamukani!). “Kodi mulidi otsimikiza kuti ndingapeze magazine onse aŵiri pa K160 yokha?” iye anafunsanso tero.

Mkaziyo anakondwera kuti Mboniyo inamlembetsera. Nanunso mungamatumiziridwe magazine a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ku keyala yanu. Tumizani K120 yokha, ndipo mudzalandira magazine onse aŵiri ameneŵa (makope atatu pa mwezi) kwa chaka chimodzi.

Chonde tumizani sabusikripishoni ya chaka chimodzi ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndatsekeramo K120 (Zambia). (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziwitso.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena