Tsamba 2
“Iwo amayendayenda m’magulu osakhala pamalo amodzi, kugona m’mapaipi a ntchito yomanga, m’madenga a nyumba zopanda anthu zokhala ndi makoswe kapena m’mbali mwa khwalala m’miulu yonyansa ya zotaidwa. Makama awo ali manyuzipepala ong’ambika, zovala zawo kokha nsanza zenizeni. Masiku awo amathera m’kuyendayenda, uchiŵereŵere ndi upandu waung’ono. Amalalira anzawo limodzinso ndi opita m’njira.” Kodi iwo ndani? Ana a m’makwalala amene amakhala mu mzinda wa Latin-America, ikusimba tero magazine ya Time. Koma iwo angakhale ana opanda kokhala a chifupifupi mzinda wina uliwonse waukulu m’dziko. Pali mamiliyoni angapo a iwo, ndipo chiŵerengero chawo chikuwonjezeka pa liŵiro lopanga mbiri.