Tsamba 2
M’zaka makumi oŵerengeka apita, munthu wasankha njira yamoyo imene yatulukapo m’kuipitsa kwakukulukulu kwa malo okhalamo zamoyo a dziko lapansi—nthaka, mitsinje, nyanja, ndi mlengalenga zaikidwa paizoni. Vutolo liridi la mitundu yonse. Monga mmene papa ananenera muuthenga wake wa Tsiku Ladziko la Mtendere (January 1, 1990) kuti: “M’zochitika zambiri ziyambukiro za malo okhalamo ndi zamoyo zimapitirira malire a Dziko limodzi palokha ; chotero yankho silingapezedwe kotheratu pa mlingo wamtundu.”—L’Osservatore Romano, December 18-26, 1989.
Kusasamala kwa munthu ponena za mtsogolo mwake kumasiyana ndi chisamaliro cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi, limene, ndiiko komwe, liri chilengedwe chake. (Yesaya 45:18) Kodi dziko laudongo nlothekera? Ngati nditero, motani ndipo liti? Nkhani zathu zapachikuto zikuyankha mafunso ameneŵa.