Tsamba 2
Kuzungulira dziko lonse, zikwizikwi za nkhani za manyuzipepala ndi magazine, limodzinso ndi maprogramu a wailesi ndi wailesi yakanema, asimba za AIDS, mliri watsopano wochititsa mantha wa nthaŵi yathu.
Chifukwa cha kufalitsidwa kumeneku ndi kuwopsya kwa AIDS, ambiri akusintha njira yawo ya moyo. Kodi kumeneku ndiko kubwerera ku makhalidwe abwino amakedzana? Kodi mapindu amene amatsogoza miyoyo yathu ali ofunika motani? Nkhani zotsegulira za mlembi wa Galamukani! mu Falansa zikusanthula mafunso ameneŵa.