Kodi Sayansi Yalitsimikizira Baibulo Kukhala Lolakwa?
Anthu ambiri lerolino amakhulupirira kuti yatero. Koma kodi yaterodi? Kodi malamulo a Baibulo pa umoyo ndi ukhondo ngachikale? Kodi bwanji ponena za cholembera cha Baibulo cha Chigumula chapadziko lonse? Kodi sayansi lachitsutsa? Kapena kodi kutumbidwa kwa mitembo youma ndi madzi ozizira oundana zikwi makumi ambiri, kuphatikizapo ya mamammoth aakulu, kwachilikiza cholembedwa cha Baibulo?
Ŵerengani umboniwo m’bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? Ilo silimakwaniritsa kokha zisulizo zonse za munthu pa Baibulo komanso limapereka malongosoledwe omvekera bwino onena za chifukwa chimene Baibulo lingavomerezedwere kukhala Mawu a Mulungu. Ulingalireni nokha umboniwo. Landirani bukhu labwino limeneli mwakudzaza ndikutumiza kapepala kotsatiraka.