Tsiku Limodzi m’Moyo Wanga mu Hong Kong Wopanikizanayo
Hong Kong ndiamodzi a malo ochulukiridwa kopambana ndi anthu m’dziko. Anthu ake mamiliyoni 5.8 okhala m’makilomitala ake 1,070 monsemonse, ali ndi anthu 5,592 pakilomitala imodzi iriyonse monsemonse. Popeza kuti 10 peresenti yokha ya dzikolo ndiimene ikukhalidwa, imeneyo ikuimira pafupifupi avareji ya 54,000 pakilomitala imodzi iriyonse monsemonse! Komabe, anthu amomwemo akuwonekera kukhala atasinthira moyamikirika kumavuto a mzinda wopanikizana, limodzi ndi malo ake okhala opanikizana, okhala ndi magalimoto ochita phokoso, ndi kuipitsidwa kwa malo.
NDINADZUTSIDWA ndi kulira kwa koloko yanga yokhala ndi belo pa 7:30 a.m., ndinadzuka pasofa pamene ndimagona, ndi kuvala mofulumira. Ndimakhala m’nyumba yaing’ono limodzi ndi makolo anga ndi alongo anga achichepere atatu, onsewo amagwira ntchito. Chotero, nthaŵi zonse pamakhala mzere womka kuchipinda chosambira, ndipo nthaŵi yathu njochepa. Pambuyo pa chakudya chofisula chamwamsanga, ndimatenga njinga yanga ndi kupalasa kumka kutireni. Vuto latsiku ndi tsiku layamba. Ndikufikira kukhala mmodzi wa anthu ambirimbiri omka kuntchito m’Hong Kong wotanganitsidwayo.
Tireni yanga imadutsa nane mofulumira m’nyumba za anthu ambiri ndi nyumba zosanja zazitali za anthu ambirimbiri. Ndiyeno ndimatuluka ndi kuloŵa m’basi kuti ndidutse doko. Timayenda kupyola m’njira za pansi panthaka, zodzala thothotho. Ha ndimpumulo wotani nanga kutulukira panja pa Chilumba cha Hong Kong kumene ofesi yanga iri, m’malo apakati a chigawo chazamalonda. Ulendo wonsewo ungachitike mkati mwa ora limodzi kufikira ku ora limodzi ndi theka, zikumadalira pakuchuluka kwa magalimoto. Potsirizira pake ndimafika 9:30. Koma palibe nthaŵi yopuma—foni imayamba kulira. Wochita naye malonda woyamba watsikulo. Ndipo zimenezo ndizimene zimandichitikira tsiku lonse lathunthu—foni ina imatsatiridwa ndi inzake, telefoni imaikidwa pansi mwakamodzikamodzi kwambiri. Kenako ndimapuma pang’ono kuti ndipeze chakudya chamasana.
Tsopano vuto ndilo kupeza pokhala mu imodzi ya makantini osaŵerengeka m’deralo. Kukuwonekera monga ngati kuti aliyense akuyesayesa kudya panthaŵi imodzi ndi pamalo amodzi ndipo mwakaŵirikaŵiri pathebulo limodzi! Kachiŵirinso ndimadyera pathebulo limodzi ndi anthu achilendo kotheratu. Ndimo mmene uliri moyo m’Hong Kong wopanikizanayo. Kenako pambuyo pa chakudya changa chamwamsanga koma chotsitsimula cha ku China, ndimabwerera kuofesi.
Ndiyenera kutsiriza ntchito pa 5:30, koma nkamodzikamodzi kuti zimenezo zimakhala zotheka. Monga momwe kunayembekezeredwa, pamene potsirizira pake ndipuma ndi kuyang’ana nthaŵi, iyo yakwana 6:15. Nthaŵi zina imakhala itapambana 7 koloko ndisanachoke. Kenako ndimayamba ulendo wobwerera kunyumba.
Choyamba ndimakwera basi, ndiyeno tireni. Potsirizira imandifikitsa pasteshoni yakwathu, ndipo ndimakatenga njinga yanga. Pamene ndipalasa kumka kunyumba, ndimakumbukira mmene tauni yathu yaing’onoyo yakulira kukhala mzinda wamakono wotanganitsidwa, womakulakulawo. Nyumba zazing’onozing’ono zakumidzi zaloŵedwa mmalo ndi nyumba zosanja zazitali, zosanjikidwa kuchokera panyumba zosanja 20 kufikira ku 30. Misewu yaikulu, yotakata yatenga malo aakulu, ndipo misewu yaikulu yapamwamba pa misewu ina ikuchulukiridwa ndi magalimoto oyenda mosalekeza aphokoso. Njira yakale ya moyo yokondweretsa yapitiratu.
Nyumba ndimalo aang’ono pang’ono—ochepera ndi mamitala 28 monsemonse kaamba ka asanu ndi mmodzi a ife ndipo ine ndiribe malo angaanga. Ndicho chifukwa chake ndimagona pasofa m’chipinda chodyera. Makolo anga ali ndi chipinda chimodzi chokha chawochawo, ndipo alongo anga atatu amagona patimibedi tosanjikana m’kachipinda kawo kakang’ono. Malo amtseri ngosatheka kupezedwa ndi ife.
Ngakhale kuti ngochepa, pali kuwongokera kwakukulu koposa amene tinali nawo kale, pamene tonsefe tinkakhala m’chipinda chimodzi pamalo a nyumba zaboma. Komatu amenewo ndiabwino kwambiri poyerekezera ndi mikhalidwe ya ena zikwi zambiri amene akukhala m’chigawo cha Mong Kok ndi amene akuchita lendi “zipinda zonga zikwere,” zosanjidwa kukhala zitatu ndi zotalika mamitala 1.8 ndi kupingasa masentimitala 76 ndi mbwambi masentimitala 76. Iwo ali ndi malo a matiresi ndi zinthu zochepa. Alibe mipando.
Podzafika 9 koloko aliyense wafika panyumba, ndipo tikukhala pansi kaamba ka chakudya chathu chamadzulo. Pambuyo pa chakudya chamadzulo winawake amatsegula TV. Imeneyo imathetsa chiyembekezo changa cha kuŵerenga mwakachetechete ndi kuphunzira. Ndimayembekezera kufikira aliyense atapita kukagona pa 11 koloko, ndiyeno ndimatsala ndekha m’chipindacho ndi ufulu wochepa wa kukhala chete ndi kusumika maganizo pamodzi. Podzafika pakati pa usiku nanenso ndimapita kukagona.
Ndakhala ndikugwira ntchito chiyambire pamene ndinasiya sukulu zaka 12 zapitazo. Tsiku lina ndidzafuna kukwatira, koma ndifunikira kugwira ntchito zolimba kuchirikiza moyo chakuti ndiribe nthaŵi yokwanira ngakhale yodziŵira bwino mkazi. Ndipo kupeza malo okhala nkovuta koposa kukwera kumwamba, monga momwe timanenera. Ngakhale kuti taphunzira kulimbana ndi mikhalidweyo, mtundu wa moyo wa m’tauni wovuta wotero sumawonekera kukhala wachibadwa kwa ine. Komabe ndikuzindikira kuti ndiri bwinopo kwambiri koposa mamiliyoni ambiri ndipo ngakhale mamiliyoni zikwi zambiri m’mbali zina zadziko amene akukhala ndi moyo popanda nyumba zabwino, magetsi, madzi a m’mipope, kapena ukhondo wokwanira. Ndithudi tifunikira dongosolo labwinopo, dziko labwinopo, ndi moyo wabwinopo.—Monga momwe yasimbidwira ndi Kin Keung.