Chitokoso kwa Makolo
Dzikoli ndimalo oipa kwambiri mwamakhalidwe koposa mmene linaliri. Pali manenanena ochuluka onena za kugonana. Magazini osonyeza akazi monga zidole wamba zoseweretsa akugulitsidwa m’sitolo yachakudya. Nyimbo ya roko imavomereza kugwirira chigololo munthu wodziŵana naye. Ndithudi, monga momwe umboni wa zimene zikuwonedwa ndi kumvedwa tsiku lirilonse ukusonyezera, lino ndidziko lachisembwere!
PROFESALA wa maphunziro abanja Greer Litton Fox ananena kuti mwa machitidwe akugonana kapena oyerekezeredwa kukhala akugonana “40 kapena chapompo” “amene munthu angasonyezedwe pawailesi yakanema kuyambira 1:30 kufikira 11 p.m. tsiku lirilonse, osakwanira 5 peresenti amaphatikizapo aŵiri okwatirana.” Pokhala zofalitsira mawu zimayesayesa kwambiri kulimbikitsa kugonana, sikodabwitsanso kuŵerenga za “ziŵerengero zazikulu kwadzawoneni ndi zotulukapo zowononga za mimba za azaka 13-19.”
Ndithudi, kwa makolo amene akufunira ana awo mtsogolo mwabwino kopambana, nchitokoso kuwalera m’dziko lachisembwere lino. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti achichepere onse akuphatikizidwa m’maunansi a kugonana. Mafufuzidwe ena akuvumbula kuti theka la asungwana a ku Amereka amsinkhu wazaka 15-19 amadziwa zakugonana, mwakutero kutsimikizira kuti theka lina silimadziwa! Ndiponso, ngakhale ambiri a awo amene anaphatikizidwa m’zakugonana akulakalaka kuti mwenzi sanatero. Wina analembera mkonzi wa nyuzipepala wina wotchedwa Ann Landers kuti:
“Kugonana kwanga ndi Joe (kutengeka maganizo kwanga koyamba) kunali kogwiritsa mwala, chotero ndinayesanso ndi Mike, ndiyeno ndi Neal, kenaka ndi George. Sindidziŵa chimene ndinali kufunafuna. Chirichonse chimene icho chinali, sindinachipeze. Ndinali nditapeza malingaliro opusa m’magazini, maprogramu osiyira panjira, ndi mu akanema. Moyo weniweni sunali wotero.
“Ngati ndikanalankhula kwa asungwana achichepere amene amaŵerenga nkhani zanu, ndikanawauza kuti kugonana kwa azaka 13-19 sikumathetsa mavuto, kumayambitsa owonjezereka. Sikumapangitsa msungwana kumva kukhala wokondedwa, kumampangitsa kumva kukhala woluluzika. Ndikanachita kuti adziwe kuti sikumapangitsa msungwana kukhala ‘mkazi weniweni,’ kungampangitse kusakhala wotero.
“Ngati ndikanalankhula kwa makolo, ndikanawalimbikitsa kugogomezera kudzilemekeza ndi kulemekeza miyezo yapamwamba.”
Kwenikweni, achichepere amene ali ndi unansi wapafupi ndi makolo awo ndi amene amadziwona kukhala otetezereka m’mabanja awo ndi kudzilingalira bwino samafulumira kukhala mikhole ya chisembwere koposa awo amene sali otero. Ndipo pali gulu la anthu oposa bwino lomwe mamiliyoni anayi kuzungulira padziko lonse lapansi mmene achichepere amathandizidwa kugwiritsitsa miyezo yapamwamba kwambiri koposa yotsatiridwa mwachisawawa lerolino.
Polingalira za zenizeni zimenezi, kodi ndimotani, mmene mungathandizire ana anu kuti adzitetezere kuchisembwere chomakulakula m’dziko lamakono? Kodi mungawathandize motani kukhala ndi moyo wachimwemwepo, wabwinopo, ndi wamakhalidwe abwinopo? Umenewo ndiwo mutu wa nkhani zathu ziŵiri zotsatira.