Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 8/8 tsamba 28
  • Kodi Apeza Helo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Apeza Helo?
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Helo Ndimalo Amtundu Wotani?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Helo ndi Wotentha?
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Kodi Helo N’chiyani Kwenikweni?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi N’chiyani Chachitikira Moto wa Helo?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 8/8 tsamba 28

Kodi Apeza Helo?

KODI mwawona kuti chiphunzitso cha helo wamoto chikuwonekera kukhala chikuzimiririka m’nthaŵi yaposachedwapa? Mwinamwake chiri chifukwa chakuti sichingapulumuke nyengo yachikaikiro imene tikukhalamo. Kapena mwinamwake anthu owonjezerekawonjezereka akuzindikira kuti lingaliro la kuzunza anthu kosatha m’moto silogwirizana ndi Mulungu wa chiweruzo cholungama ndi wachikondi wofotokozedwa m’Baibulo. Chirichonse chimene chiri chifukwa cha kusakhulupililira, atsogoleri ena achipembedzo akulabadira mwa njira zimene zimasonyeza kuthedwa nzeru. Talingalirani mfundoyo.

Mu United States, zonse ziŵiri matelevizheni “Achikristu” a m’dzikolo ndi nyuzipepala yachipembedzo posachedwapa inasimba kuti asayansi atulukira “helo” pamene anali kukumba m’Siberia! Magazini otchedwa kuti Biblical Archaeology Review mogwiritsidwa mwala inafotokoza mwachidule nkhani ina yotero.

Kukunenedwa kuti, kagulu ka asayansi a ku Finland ndi a ku Norway kanali ku Siberia kukumba pansi pamgodi kuti awone zimene angapeze. Iwo anadabwa kwambiri pamene, makilomitala angapo pansi pawo, anawona nchokoto wa makina okumbira unayamba kuzungulira mmalo apululu! Iwo anadabwa mowonjezereka pamene anapeza kuti kutentha kwa pansipo kunali koposa madigiri a Celsius 1,100! Komabe, anadabwa kopambana, pamene anatsitsira chokuzira mawu m’dzenjemo ndi kumva mawu zikwi zambiri—mwinamwake mamiliyoni ambiri—a anthu, onse akumabuula ndi ululu! Nkhaniyo ikupitirizabe kuti, asayansiwo anawopa kwambiri, kotero kuti ambiri anasiya ntchitoyo. Ena analumbira kusunga chinsinsi, pamene enanso anatembenuzidwa kuchoka pa kukhala osakhulupirira Mulungu kumka ku “Chikristu” chifukwa cha umboni wa helo umenewu.

Nzosadabwitsa kuti, awo amene anasindikiza ndi kubwereza nkhani imeneyi ananena kuti inalembedwa bwino lomwe. Rich Buhler, wotsogoza makambitsirano a pawailesi, analemba mu Christianity Today kuti iye ndi antchito ake anayesa kufufuza malipoti oterowo. Pakufufuzako anapeza kuti, magwero amodzi anali ndi nkhani zimene zinafalitsidwa zomwe zinagwira mawu makalata amenenso anagwira mawu nkhani zopanda umboni.

Magwero ena anali kalata yochokera kwa mwamuna wa ku Norway amene, pofunsidwa, anavomereza poyera kuti kalata yake inali yongopeka. Iye anaitumiza kokha chifukwa chakuti anali wotsimikiza kuti ikakhulupiriridwa ndi kufalitsidwa. Mosakaikira iye anazindikira chowonadi chomvetsa chisoni chakuti magulu achipembedzo ambirimbiri—amakhulupirira zimene amafuna kukhulupirira.

M’Malemba Achihebri a Baibulo liwu lakuti “helo” latembenuzidwa kuchokera kuliwu Lachihebri lakuti sheol. Limapezeka nthaŵi 65 ndipo m’matembenuzidwe Abaibulo a Authorized King James likutembenuzidwa nthaŵi 31 kukhala “helo,” nthaŵi 31 kukhala “manda,” ndipo nthaŵi 3 kukhala “dzenje.” M’Malemba Achigiriki a matembenuzidwe Abaibulo amenewo liwulo “helo” likutembenuzidwa kuchokera kuliwu Lachigiriki lakuti Hades mmalo ake onse khumi mmene likupezeka. Mawu onse aŵiri lakuti sheol ndi lakuti hades amatanthauza manda wamba a anthu, ndipo samasonya konse kuululu kapena chizunzo chamoto kapena kwa aliyense wokhala ndi moyo makilomitala angapo pansi pa nthaka ya ku Siberia!

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

Picture Book of Devils, Demons and Witchcraft/Ernst ndi Johanna Lehner/Dover

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena