Kuyamikira “Galamukani!”
OŴERENGA magazini ano owonjezerekawonjezereka amayamikira chidziŵitso chimene amalandira pankhani zochuluka kwambiri. Kumwera kwa France mwamuna wina ndi mkazi wake amene ali Mboni za Yehova analandira kalata yotsatirayi yochokera kwa bwana wina amene iwo anasiira kope la Galamukani!
“Bambo ndi Mayi Okondedwa:
“Ndidziŵa bwino lomwe kuti Mulungu ali ndi zinthu zina zozichita zosakhala kukhutiritsa njira zathu zazing’onong’ono zoseketsa zowonera kuphatikizidwa kwake mumkhalidwe uliwonse wothekera. Ngakhale kuti inemwinine sindimachirikiza mtundu umenewu wa kulingalira, ndiri wotsimikizira kuti kufika kwanu pamene ndinali kuchoka panyumba sikunali kwamalunji. Ndinali kokha ndi nthaŵi yolandira kope la August 8, 1990, la Galamukani! Kukanakhala kogwiritsa mwala chotani nanga kuphonya!
“Kupenda kwanzeru mpambo wa nkhani zakuti ‘Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamuyeso’ kunadzutsa chikondwerero changa ndipo kunandidabwitsa kwambiri. Ndikuchirikiza mwamphamvu njira imene mpambowo waperekedwera. . . . Chifukwa chake, ndikupempha chonde kuti mulinganize kuti ndidzilandira makope alinkudza a Galamukani! Sindifuna kuphonya lirilonse lokhala ndi mpambo umenewu.”
Mboni za Yehova ndizo gulu la m’mitundu yonse la ophunzira Baibulo oposa mamiliyoni anayi amene ali odzipereka kuthandiza anthu kuphunzira zowonjezereka ponena za dziko loŵazungulira ndi ponena za Mawu a Mulungu ndi mmene akukwaniritsidwira. Ngati mungakonde kudziŵa zowonjezereka kapena phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena keyala yoyenerera pa ondandalitsidwa pa tsamba 5.