Munthu Wamba
“ANABADWIRA m’mudzi wosatchuka, mwana wa mkazi wakumidzi. Koma anakulira m’mudzi wina, kumene anagwirako ntchito m’malo opalira matabwa kufikira pamene anali ndi zaka makumi atatu. Ndiyeno kwazaka zitatu iyeyu anakhala mlaliki woyendayenda.
“Sanalembe buku. Sanakhale ndi udindo. Analibe banja kapena nyumba. Sanapite kukoleji. Sanapite kukawona mzinda ulionse waukulu. Sanayende ulendo wa mamailo mazana aŵiri kuchokera kumene anabadwira. Sanachite chilichonse cha zinthu zimene munthu amachigwirizanitsa ndi kupambana. Sanapatsidwe ulemu uliwonse koma anangokhala munthu wamba.
“Anali wa zaka makumi atatu mphambu zitatu zokha pamene anthu anamtembenukira. Mabwenzi ake anathaŵa. Anaperekedwa kwa adani ake ndi kuimbidwa mlandu momtonza. Anakhomeredwa pa [mtengo] pakati pa mbala ziŵiri. Pamene anali kufa, amene anamuphawo anachitira maere zovala zake, zinthu zokha zimene anali nazo padziko lapansi. Pamene anafa, anaikidwa m’manda obwereka mwa kumva chisoni kwa bwenzi lake.
“Zaka mazana khumi ndi zisanu ndi zinayi zafika ndi kupita, ndipo lerolino munthuyo akali phata la mtundu wa anthu, mtsogoleri wa kukhalapo kwa anthu. Magulu onse ankhondo amene anaguba, magulu onse a ankhondo apamadzi amene anakhalako, nyumba zonse zamalamulo zimene zinakhalako, mafumu onse amene analamulira kunja kuno, ataikidwa pamodzi, sanayambukire moyo wa anthu papulaneti lino kwambiri koposa munthu wamba ameneyo.”a—Ndemanga zochokera kwa munthu wosadziŵika paumoyo wa Yesu Kristu.
[Mawu a M’munsi]
a Tsatanetsatane wa munthu wamba ameneyo ali m’buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.