Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 9/8 tsamba 32
  • Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
  • Galamukani!—1993
Galamukani!—1993
g93 9/8 tsamba 32

Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo

Chaka chatha Mboni za Yehova zinafalitsa trakiti lamasamba asanu ndi limodzi lokhala ndi mutu wapamwambapawu. Moyenerera, limapereka mtundu wa chithandizo chimene opsinjika maganizo amafuna. Trakitilo limasonyeza kuti Baibulo ndilo magwero abwino koposa a chitonthozo. Limasonyeza Malemba ambiri oyenerera pankhani ya kupsinjika maganizo, kuphatikizapo amene angagwiritsiridwe ntchito kuthandiza anthu opsinjika maganizo.

M’chilimwe chapita ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova mu Rome, Italy, inalandira foni mu imene woimba foniyo anati: “Ndikufuna kukuthokozani chifukwa cha trakiti lonena za kupsinjika maganizo. Ndangolilandira kumene, ndipo ndikumva kukhala woumirizika kukuthokozani. Sindinayambe ndaŵerengapo kanthu kena kolimbikitsa chotere m’buku lina lililonse la zamankhwala. Ndikufuna kukuyamikirani chifukwa chakuti mwakhoza kufotokoza zinthu zambiri m’kadanga kakang’ono.

“Pamene ndinaŵerenga trakitili, ndinalira. Ndikufuna kukulimbikitsani kupitirizabe ntchito yanu. Njofunika; muyenera kuichita mu Italy monse ndi padziko lonse.”

Ngati mukufuna kope la trakiti limeneli, Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo, kapena mawu owonjezereka, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena kukeyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena