Chifukwa Chake Mabishopu a Italy Akuda Nkhaŵa
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY
MU November 1993 pa msonkhano wa mabishopu Achitaliyana pananenedwa ndemanga zambiri zodana ndi Mboni za Yehova. Kunanenedwa kuti sizinali Akristu ndi kuti kulalikira kwawo kwa kukhomo ndi khomo kunali “kutembenuza anthu kwankhanza.”
Komabe, si akuluakulu a zipembedzo onse amene akuvomereza. Mwachitsanzo, Attilio Agnoletto, profesa wa mbiri yakale ya Chikristu pa Milan State University, akufotokoza Mboni za Yehova kukhala “gulu lamphamvu, lolingalira kwambiri, logwirizana ndi Baibulo, lovomerezeka kotheratu limene lilibe chilichonse chosakhala cha Chikristu.”
Ndipo bwanji nanga za “kutembenuza anthu kwankhanza” kwawoko? “Mawuwo ‘kwankhanza’ ngosayenera konse,” profesa Agnoletto anauza Galamukani! motero. “Zimenezi zingatanthauze kuti kutembenuza anthu kwa Yesu Kristu kunalinso ‘kwankhanza.’”
Kodi nchifukwa ninji mabishopu ali ndi udani wotero pa Mboni za Yehova? Profesa Agnoletto akulingalira kuti kutsutsa kwawoko “kukuchititsidwa ndi kuchuluka ndi chipambano cha Mboni za Yehova mu Italy lerolino,” chimene, iye akuwonjezera motero, “chikuchitikira limodzi ndi vuto lachipembedzo cha Katolika.”
Lerolino atsogoleri achipembedzo amafuna kusuliza ndi kupinga awo amene amamvera lamulo la Yesu la kulalikira. (Mateyu 28:19, 20; yerekezerani ndi Mateyu 5:11, 12.) Nyuzipepala yotchedwa La Stampa ikusimba kuti mosasamala kanthu za chitsutsocho, Mboni za Yehova zili chipembedzo chachiŵiri chachikulu koposa mu Italy, chimene tsopano chili ndi anthu oposa 200,000 ndipo akupitirizabe kuwonjezereka.
Mosiyana ndi zimenezo, Tchalitchi cha Katolika chakhala ndi kutsika kwa ofika kutchalitchi m’zaka zaposachedwapa. Chotero kuchiyambi kwa 1994, Papa John Paul II analimbikitsa Akatolika Achitaliyana kukhala alaliki okangalika, akumalalikiradi khomo ndi khomo—monga momwe Mboni za Yehova zimachitira!a
[Mawu a M’munsi]
a Onani tsamba 10.