Galamukani! Maziko a Mayeso
PAMENE ana a sukulu m’dziko la Suriname ku South America anatsegula kabuku kawo ka mayeso opitira ku sukulu ya sekondale m’July 1993, anaona kuti oŵerenga nthaŵi zonse magazini a Galamukani! anachita mwaŵi. Chifukwa chake nchakuti pafupifupi theka la mafunso m’kabukuko ka masamba 36, kamene kanakonzedwa ndi Ministry of Education’s Examination Bureau, anazikidwa pa nkhani ziŵiri za mu Galamukani!
Kuchokera patsamba 1 mpaka tsamba 9 panali nkhani yakuti “Mashantikompaundi—Nthaŵi Zovuta m’Chipwirikiti cha m’Tauni” imene inali mu Galamukani! wa October 8, 1992. Panali mafunso 21 amene anayesa munthu pa kumvetsa kwake nkhaniyo. Pamasamba 10 mpaka 16 a kabuku kamayesoko panali mafunso 14 pankhani yakuti “The Capybara—Mistake or Marvel of Creation?” imene inali mu Awake! ya September 22, 1992.
“Mwa kugwiritsira ntchito nkhani zimenezi kuyesa kumvetsa nkhani kwa ana asukulu m’dziko lonselo,” anatero hedimasitala wina m’dera lakumadzulo la Suriname, “akuluakulu asukulu amasonyeza kuti amaona Galamukani! monga chitsanzo cha galamala yolongosoka ndi kalembedwe kabwino.”
Ngati mungafune kope la Galamukani! kapena kuti munthu wina adzafike panyumba kudzakambitsirana nanu za nkhaniyi, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pa ondandalikidwa patsamba 2.