Kumene Ndalama Zimakhala m’Mitengo
TINENE kuti ndalama zimamera m’mitengo ndi kuti inu muli ndi mtengo wotero. Tsopano talingalirani kuti mtengo wanuwo unamera m’mbali mwa njira imene anansi anu ambiri amayendamo tsiku lililonse. Kodi muganiza kuti ndalamazo zingakhale kwautali wotani mu mtengo wanu?
Ngati anansi anu onse ndi Mboni za Yehova, mtengo wanu wa ndalama ungakhale wosungika. Chifukwa ninji tikunena tero? Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimatsatira lamulo la Baibulo la kukhala oona mtima pa zinthu zonse. (Ahebri 13:18) Chochitika cha posachedwapa chikusonyeza zimenezi.
Ku Nigeria, West Africa, ndalama yokwanira manaira asanu yapepala inapezeka pamsewu mamita 91 kuchokera pa nyumba yapafupi kwambiri ya ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society. Woipezayo anaimangirira kunthambi ya mtengo wa ngole wapafupipo, akumaganiza kuti munthu wotaya ndalamayo angabwere kudzaifunafuna.
Ngakhale kuti ndalamayo inali kuonekera bwino kwa Mboni za Yehova zambiri zimene zinali kudutsa pamenepo tsiku ndi tsiku, palibe amene anadzaitenga. Patapita masiku ambiri inachotsedwapo ndi kuikidwa m’bokosi la zopereka la Sosaite.