Anthu Ambiri Amakhala ndi Moyo ndi Kufa mu Umphaŵi Wadzaoneni!
YATI amachokera kwawo ku matauni a zithando m’dziko lina la kummwera koma chakummaŵa kwa Asia kupita ku fakitale kumene amasoka zidutswa za chikopa ndi nsambo za nsapato. Pantchito ya mwezi umodzi—maola 40 mlungu uliwonse ndiponso maola 90 a ovataimu—amapeza ndalama zosakwana $80. Kampani yopanga nsapato yomlemba ntchito mkaziyo monyadira imapereka chithunzi chakuti imachirikiza mwakhama zoyenera za anthu m’maiko omatukuka. Kumaiko a Kumadzulo, kampani imeneyi imagulitsa nsapato zake pamtengo woposa $60 peyala imodzi. Malipiro amenewo amakwana mwinamwake $1.40 chabe ya mtengo umenewu.
“Pochoka m’fakitale yaudongo yamagetsiyo,” ikutero nkhaniyo mu Boston Globe, Yati “amangokhala ndi ndalama zokwana kulipirira lendi kakhumbi ka mamita 3 m’lifupi ndi 3.6 m’litali, ka makoma auve odzala abuluzi. Mulibe mipando kapena mibedi, choncho Yati ndi anzake aŵiri amagona pansi pa mataulosi ndi dothi atadzipinda.” Nzachisoni kuti sindiye yekha amene ali mumkhalidwe umenewu.
“Kodi anthuwa amapeza bwino chifukwa cha ine kapena ayi?” akuŵiringula motero mkulu wina wa malonda. “Malipiro ochepawo amawakhozetsa kusangalala ndi moyo wabwinopo. Iwo sangakhale ndi moyo wa mwana alirenji, komatu sakufa ndi njala.” Komabe, iwo nthaŵi zambiri amasoŵa chakudya, ndipo kaŵirikaŵiri ana awo amagona ndi njala. Masiku onse moyo wawo umakhala pachiswe chifukwa cha malo angozi omwe amagwirako ntchito. Ndipo ambiri alikufa imfa ya pang’onopang’ono chifukwa chogwira poizoni ndi zotayidwa zina zakupha. Kodi umenewo ndi “moyo wabwinopo”?
Hari, wantchito pafamu ina kummwera kwa Asia, anaona nkhaniyo mosiyana. Anafotokoza bwino lomwe ndi mawu okuluŵika mkhalidwe womzinga womvetsa chisoni wa moyo kapena imfa. “Pakati pa mtondo ndi munsi,” iye anatero, “tsabola amaphwanyika. Ife amphaŵi tili ngati tsabola—chaka chilichonse amatisinja, ndipo posapita nthaŵi sipamatsala kanthu.” Hari sanakhalepo ndi “moyo wabwinopo,” ngakhale kuudziŵa nkomwe moyo wa mwana alirenji umene mwinamwake omlemba ntchito anali nawo. Patapita masiku angapo, Hari anafa—munthu wina wakufa muumphaŵi wadzaoneni.
Anthu ochuluka amakhala ndi moyo ndi kufa monga Hari. Amangovutika, posoŵeratu chochita, pamene amakakamizidwa m’mikhalidwe imene imawafoola. Ndi yani? Kodi ndi anthu otani amene angachite zimenezi? Anthu ooneka kukhala othandiza. Amati akufuna kupezera mwana wanu chakudya, kuthandizira dzinthu zanu kukula, ndi kutukula moyo wanu, kukulemeretsani. Kwenikweni, amafuna kudzilemeretsa iwo eni. Iwo amaona mpata wogulitsira zinthu zawo, ndi wopezerapo phindu. Ngati zotulukapo za umbombo wawo zikhala ana anjala, antchito oloŵedwa poizoni, ndi malo oipitsidwa, alibe nazo kanthu. Ndiwo mtengo umene makampani akufuna kulipira kaamba ka umbombo wawo. Chotero pamene mapindu awonjezereka, nazonso ziŵerengero za akufa zoswa mtima zimawonjezereka.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzithunzi cha United Nations 156200/John Isaac