Chiŵiya Chofunika kwambiri cha Maphunziro
Phungu wa nyumba ya malamulo wina ku dziko la Sri Lanka analembera “Mkonzi wa ‘Galamukani!’” Kalata yake yajambulidwa pansipa:
“Bwana Wokondedwa,
“Ndiyenera kunena kuti ngakhale kuti magazini a Galamukani! amene mumafalitsa ndi aang’ono, iwo ngwofunikadi ndipo amakhala apanthaŵi yake. Nkhani iliyonse imathandizira wachichepere wa m’tsiku lino kusiyanitsa bwinobwino chabwino ndi choipa.
“Ndaŵerenga nkhani zonse. Zimene ndaona nzakuti mphunzitsi wapasukulu aliyense, wophunzira, ndi kholo ayenera kuŵerenga magazini ameneŵa mosakayikira.
“Ndikuyamikira kwambiri ntchito yabwino imene mukuchita. Ndikukufunirani chipambano pa zoyesayesa zanu.”
Pafupifupi magazini mamiliyoni 16 a kope lililonse la Galamukani! amasindikizidwa, m’zinenero 78. Magaziniwa amadziŵika dziko lonse lapansi monga chiŵiya chofunika kwambiri cha maphunziro. Inunso mudzapindula mwa kuwaŵerenga. Ngati mungafune kope kapena ngati mungafune kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalitsidwa patsamba 5.