Masoka Achilengedwe—Kuthandiza Mwana Wanu Kulimbana Nawo
ZIVOMEZI, akavuluvulu, moto, kusefukira kwa madzi, mikuntho—mmenedi timakhalira opanda thandizo nanga pamene tiyang’anizana ndi ukali wa chilengedwe! Kaŵirikaŵiri achikulire amapeza kuti pamapita zaka kuti zithunzithunzi zowopsazo zokhomerezeka m’maganizo chifukwa cha kukumana ndi tsoka lachilengedwe ziyambe kuzimiririka. Mosadabwitsa, ana angafunikire chithandizo chowonjezereka kuti aiŵale zokumana nazo zotero.
Federal Emergency Management Agency (FEMA) ya ku United States imanena kuti mwamsanga pambuyo pa tsoka, mwachibadwa ana amawopa kuti (1) adzasiyidwa okha, (2) adzasiyanitsidwa ndi banja, (3) chochitikacho chidzabwerezanso, ndipo (4) wina wake adzavulazidwa kapena kuphedwa. Kodi inu monga kholo mungachitenji kuti muchepetse nkhaŵa ya mwana wanu pambuyo pa tsoka? FEMA ikupereka malingaliro awa.a
Yesetsani kuchititsa banja kukhala pamodzi. Kukhala pamodzi kumapereka chitsimikiziro kwa mwana wanu ndipo kumathetsa mantha ake akuti angasiyidwe. Kuli bwino kusasiya ana kwa achibale kapena mabwenzi kapena pamalo opulumukirako pamene mukufunafuna thandizo. “Ana amada nkhaŵa,” ikutero FEMA, “ndipo adzada nkhaŵa kuti kapena makolo sadzabweranso.” Ngati mufunikira kupita kwina kwake, pitani ndi mwana wanu ngati kuli kotheka. Mukatero “mwana [wanu] sadzakhala woumirira kwambiri.”
Patulani nthaŵi ya kufotokoza mofatsa ndi motsimikizira. Uzani mwana wanu zimene mumadziŵa ponena za tsokalo. Ngati nkofunika, bwerezani kufotokoza kwanu nthaŵi zingapo. Tchulani zimene zidzachitika pambuyo pake. Mwachitsanzo, munganene kuti, ‘Usiku walero tonse tidzakhala pamodzi m’nyumba yothaŵiramo.’ Lankhulani ndi ana mwachindunji, mukumagwada pansi ngati nkofunika.
Limbikitsani mwana wanu kulankhula. “Kulankhulana nkofunika kwambiri pa kuchepetsa nkhaŵa ya mwana,” FEMA ikutero. Mvetserani zimene mwana aliyense akuuzani ponena za tsokalo ndi zimene akuwopa. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:19.) Muuzeni kuti kuchita mantha nkwachibadwa. Ngati mwana wanu sakuoneka kukhala wofunitsitsa kulankhula, mdziŵitseni kuti inu muli ndi mantha. Kuchita motero kungamchititse kufotokoza mantha ake mosavuta, chotero zikumachepetsa nkhaŵa yake. (Yerekezerani ndi Miyambo 12:25.) “Ngati nkotheka, phatikizanipo banja lonse pa makambitsirano amenewo.”
Phatikizanipo ana pantchito zoyeretsa. Pamene mukuyeretsa ndi kukonza nyumba, patsani ana ntchito yawo. “Kukhala ndi ntchito kudzawathandiza kuzindikira kuti zonse zidzakhala bwino.” Komabe, mwana wamng’ono kwambiri kaŵirikaŵiri amafunikira chisamaliro chapadera. FEMA ikufotokoza kuti: “Mwana wotero angafunikire chisamaliro chakuthupi chowonjezereka, kumkupatira kwambiri; ndipo zimenezi zimachititsa kukhala kovuta kwa makolo kusamalira zinthu zina zimene ziyenera kuchitidwa. Mwatsoka, palibe chidule. Ngati zofunikira za mwana sizinakwaniritsidwe, vutolo lidzatenga nthaŵi yaitalipo.”
Mfundo ina yomalizira iyenera kukumbukiridwa. FEMA ikulangiza makolo kuti: “Kwenikweni, muyenera kudziŵa zimene zikufunika kwambiri kwa mwana wanu.” Kugwiritsira ntchito zitsogozo zimenezi kungakuthandizeni kuchita zonse zimene mungathe pamkhalidwe wovuta.
[Mawu a M’munsi]
a Otengedwa m’mabuku akuti Helping Children Cope With Disaster ndi Coping With Children’s Reactions to Hurricanes and Other Disasters, ofalitsidwa ndi FEMA.