Chimene Anali Kufuna Ndicho Kuona Mtima
Mkazi wachichepere ku Ecuador anapita ku mayeso a ntchito. Atakambitsirana ndi ena ofunanso ntchito—onse anali 36—anazindikira kuti anali ndi mwaŵi wochepa wa kupeza ntchito. Iwo anali kudziŵa ntchito ndipo anali akuyunivesite, pamene iye analibe zonsezo. Ndipo pa mafunso asanu ndi limodzi amene anafunsidwa, iye analephera aŵiri. Komabe, funso limodzi linakhudza zaumwini: “Kodi kwa iwe choonadi nchiyani?”
Mkaziyo anayankha kuti: “Choonadi si nthanthi koma ndi chinthu chimene tiyenera kutsatira. Tiyenera kulankhula choonadi ndipo osanama, pakuti ngati tinama, timatsatira Satana Mdyerekezi. Ngati tilankhula choonadi, timakondweretsa Mulungu ndipo timapeza mapindu aumwini ambiri.”
Pamene manijala anafunsa mkaziyo za chipembedzo chake, iye anati anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Tsiku lotsatira anauzidwa kuti wasankhidwa kuloŵa ntchito. Patapita mwezi umodzi mkaziyo anafunsa manijalayo chimene anamsankhira, ndipo iye anati chinali chifukwa cha kuona mtima kwake.
Kodi si zoona kuti anthu ambiri lerolino ali osaona mtima? Komabe, anthu amene amalemekeza Baibulo amadziŵika chifukwa cha kuona mtima kwawo. Magazini a Nsanja ya Olonda ya July 1, 1995, anati: “M’Baibulo, ‘choonadi’ sichili konse monga lingaliro losamvetsetseka ndi losatsatirika limene afilosofi amakanganapo.”
Mudzapindula mwa kuŵerenga Nsanja ya Olonda nthaŵi zonse, imene imadziŵika padziko lonse monga mchirikizi wa choonadi cha Baibulo. Ngati mukufuna kukhala ndi kope kapena kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pandandanda ya patsamba 5.