Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 32
  • “Ungachite Bwino Kwambiri Kuona Galamukani!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ungachite Bwino Kwambiri Kuona Galamukani!”
  • Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 32

“Ungachite Bwino Kwambiri Kuona Galamukani!”

ZIMENEZO nzimene Pasquale, Mboni ya Ye- hova yachichepere imene inali kuchita kosi pa koleji ku Bari, Italy, inauzidwa pamene inape- mpha mphunzitsi wake wazamaganizo ma- notsi ena amene anali nawo onena za ku- mwerekera ndi anamgoneka. Komabe, kale mphunzitsi ameneyu anali woipidwa ndi Mboni za Yehova. Kodi nchiyani chinapa- ngitsa mkhalidwe wakewo kusintha?

Pasquale anafotokoza kuti: “Pamape- to a phunziro, mphunzitsiyo anape- mpha ophunzira ake kumthandiza kupe- za nkhani zonena za kuchitira nkhanza mwana, phunziro limene anali kukonze- kera zowonjezerapo titamaliza maphunziro. Ndinakumbukira makope angapo a Galamukani! amene anasimba zime- nezi ndi nkhani zina zogwirizana nazo, monga yakuti ‘Maphunziro Azakugonana—Kodi Ndani Ayenera Kuwapereka?’ (March 8, 1992). Komabe, pozindikira kuipidwa kwa mphunzitsi wanga ndi Mboni, ndinape- mpha mnzanga wa m’kalasi kumpatsa magaziniwo.”

Pasquale akufotokoza zimene zinachitika pamene, patapita masiku angapo, anapempha mphunzitsi wake kumpatsa manotsi amene anafuna pa nkhani ya kumwerekera ndi anamgoneka: “Sanayankhe nthaŵi yomweyo. M’malo mwake mphunzitsi wachikaziyo anaimirira nadza kudzandigwira chanza. Iye anati poyamba sanafune kulandira magazini a Mboni za Yehova chifukwa ankawaona kukhala osagwira mtima kwambiri ndi achibwana. Komabe, atawaŵerenga, anasintha maganizo. Ananena kuti anapeza nkhani za magaziniwo kukhala zothandiza koposa m’chitaganya. Anati adzaphatikiza mfundo za mu Galamukani! pa zofufuza zake zowonjezera.”

Bwanji nanga za pempho la Pasquale la manotsi a kuledzera ndi anamgoneka? “Ndikupatsadi ndi mtima wonse,” mkaziyo anatero, “koma ungachite bwino kwambiri kuona Galamukani! Ndiwo magazini amene ali ndi nkhani zofunika, ndipo ngothandiza, ngakhale pa mlingo wa yunivesite.”

Galamukani! amasimba za mavuto amakono ndipo amayesayesa kupereka thandizo logwira ntchito kwa awo amene akuyang’anizana ndi mavuto aakulu kapena aang’ono m’moyo watsiku lililonse. Ngati mukufuna kudziŵa thandizo limene Baibulo lingapereke, onanani ndi Mboni za Yehova, zimene zimagaŵira Galamukani!, kapena lemberani ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena