Kodi Mumadziŵanji Ponena za Yesu?
Ponena za Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, buku lokhala ndi zithunzi lamasamba 448 lonena za moyo wa Yesu Kristu, mkazi wina wazaka 84 wa ku United States anati: “Ndaŵerenga Baibulo lonse nthaŵi zosiyanasiyana, ndipo Munthu Wamkulu wandithandiza kumvetsetsa kuŵerenga kwanga Baibulo.” Bukulo limapangitsa nkhani za m’Baibulo za moyo wa Yesu kukhala zenizeni kwa iye.
“Sindimatopa kuliŵerenga bukulo,” analemba choncho. Ndaliŵerenga nthaŵi zisanu ndi ziŵiri ndipo ndayamba kuliŵerenganso. Ndimayamikira ndi mtima wonse mikhalidwe yodabwitsa ya Yesu. Pamene ndiŵerenga mitu yonena za mlungu wotsirizira wa Yesu padziko lapansi, ndimaŵaŵidwa ndi nkhanza imene anachitidwa, makamaka m’maola ake otsiriza, ndiponso ndi imfa yake pamtengo wozunzirapo. Komabe, analemekeza Atate wathu wakumwamba, Yehova.”
M’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, tayesetsa kupereka chochitika chilichonse cha moyo wa Yesu wapadziko lapansi chimene chinalembedwa m’Mauthenga Abwino anayi. Lingakuthandizeni kuphunzira zambiri ponena za Yesu. Ngati mungakonde kulandira kope kapena mungafune phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.