Usiku Woyenera Kuukumbukira
SANDE, MARCH 23, 1997
USIKUWO Yesu Kristu asanafe, anayambitsa pamodzi ndi atumwi ake chikumbutso cha imfa yake. Ali pachakudya chopepuka pamene anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa monga zizindikiro, Yesu analamula kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Mboni za Yehova zikukupemphani mokoma mtima kuti mudzachite nazo pamodzi Chikumbutso cha chaka ndi chaka chimenechi. Chaka chino chidzachitidwa dzuŵa litaloŵa pa Sande, March 23, deti limene limagwirizana ndi Nisani 14 pa kalenda yamwezi ya Baibulo. Chonde funsani Mboni za Yehova za kwanuko ponena za malo enieni osonkhanira ndi nthaŵi yake.