“Linali Buku Loyamba Limene Anaŵerengapo”
Mboni za Yehova ku Ukraine zimalankhula kaŵirikaŵiri ndi anthu omadikira sitima. Mkazi wina yemwe anachita chidwi ndi Baibulo anapatsidwa buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, chofalitsa chokhala ndi zithunzithunzi zambiri zolongosola mwatsatanetsatane mbiri ya Baibulo.
Tsiku lina, pasiteshoni imodzimodziyo, mkaziyo anaionanso Mboni ija naithokoza chifukwa cha bukulo, akumafotokoza kuti: “Mwana wanga sanali kufuna kuŵerenga mabuku ake a kusukulu. Sanawaŵerengepo ngakhale pang’ono. Koma nditangompatsa buku lija la Nkhani za Baibulo, anakhumba kwambiri kuliŵerenga. Anaŵerenga buku lonse pamilungu ngati iŵiri. Linali buku loyamba limene anaŵerengapo. Koma koposa zonse, anakondwera kudziŵa Mulungu. Ndipo ine ndemwe ndikukondwera kumuona akusintha. Chonde ndipatseni zinanso zoŵerenga.”
Mkazi winanso anali atangoima chapafupi ndiye anaimva nkhaniyo. Nayenso anapempha kope la Buku Langa la Nkhani za Baibulo. Inunso mungapeze buku limeneli lamasamba 256 kapena wina angabwere kwanu kudzakambitsirana nanu ubwino wa phunziro la Baibulo, mwa kulembera ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena kukeyala yapafupi nanu ili patsamba 5.